Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 29:15-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndinali maso a akhungu,Ndi mapazi a otsimphina.

16. Ndinali atate wa waumphawi;Ndi mlandu wa iye amene sindinamdziwa ndinafunsitsa.

17. Ndipo ndinatyola nsagwada ya wosalungama,Ndi kukwatula cogwidwa kumano kwace.

18. Pamenepo ndinati, Ndidzatsirizika m'cisa canga;Ndipo ndidzacurukitsa masiku anga ngati mcenga.

19. Muzu wanga watambalala kufikira kumadzi;Ndi mame adzakhala pa nthambi yanga usiku wonse.

20. Ulemu wanga udzakhala wosaguga mwa ine,Ndi uta wanga udzakhala wosalifuka m'dzanja mwanga.

21. Anthu anandimvera, nalindira,Nakhala cete, kuti ndiwapangire.

22. Nditanena mau anga sanalankhulanso,Ndi kunena kwanga kunawakhera.

23. Anandilindira ngati kulindira mvula,Nayasama pakamwa pao ngati kulira mvula ya masika.

24. Ndinawaseka akapanda kulimbika mtima;Ndipo sanagwetsa kusangalala kwa nkhope yanga.

Werengani mutu wathunthu Yobu 29