Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 29:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Pakuti ndinapulumutsa wozunzika wakupfuula;Mwana wamasiye yemwe wosowa mthandizi.

13. Dalitso la iye akati atayike linandidzera,Ndi mtima wa mkazi wamasiye ndinauyimbitsa mokondwera.

14. Ndinabvala cilungamo, ndipo cinandibvala ine;Ciweruzo canga cinanga mwinjiro ndi nduwira.

15. Ndinali maso a akhungu,Ndi mapazi a otsimphina.

16. Ndinali atate wa waumphawi;Ndi mlandu wa iye amene sindinamdziwa ndinafunsitsa.

17. Ndipo ndinatyola nsagwada ya wosalungama,Ndi kukwatula cogwidwa kumano kwace.

18. Pamenepo ndinati, Ndidzatsirizika m'cisa canga;Ndipo ndidzacurukitsa masiku anga ngati mcenga.

19. Muzu wanga watambalala kufikira kumadzi;Ndi mame adzakhala pa nthambi yanga usiku wonse.

Werengani mutu wathunthu Yobu 29