Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 28:7-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Njira imeneyi palibe ciombankhanga ciidziwa;Lingakhale diso la kabawi losapenyapo.

8. Nyama zodzikuza sizinapondapo,Ngakhale mkango waukali sunapitapo.

9. Munthu atambasulira dzanja lace kumwala;Agubuduza mapiri kuyambira kumizu.

10. Asema njira pakati pa matanthwe,Ndi diso lace liona ciri conse ca mtengo wace.

11. Atseka mitsinje ingadonthe;Naturutsira poyera cobisikaci.

12. Koma nzeru, idzapezeka kuti?Ndi luntha, malo ace ali kuti?

13. Munthu sadziwa mtengo wace;Ndipo silipezeka m'dziko la amoyo.

14. Pozama pakuti, Mwa ine mulibe;Ndi nyanja ikuti, Kwa ine kulibe.

15. Silipezeka ndi golidi,Sayesapo siliva mtengo wace.

16. Sailinganiza ndi golidi wa Ofiri,Ndi sohamu wa mtengo wace wapatali kapena safiro.

Werengani mutu wathunthu Yobu 28