Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 28:3-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Munthu athawitsa mdima,Nafunafuna mpaka malekezero onse,Miyala ya mdima wa bii ndi ya mthunzi wa imfa.

4. Aboola mgodi posiyana patali pokhala anthu;Aiwalika ndi phazi lopitapo;Apacikika kutali ndi anthu, nalendewa-lendewa.

5. Kunena za nthaka, kucokera momwemo mumaturuka cakudya,Ndi m'munsi mwace musandulizika ngati ndi moto.

6. Miyala yace ndiyo malo a safiro,Ndipo iri nalo pfumbi lagolidi.

7. Njira imeneyi palibe ciombankhanga ciidziwa;Lingakhale diso la kabawi losapenyapo.

8. Nyama zodzikuza sizinapondapo,Ngakhale mkango waukali sunapitapo.

9. Munthu atambasulira dzanja lace kumwala;Agubuduza mapiri kuyambira kumizu.

10. Asema njira pakati pa matanthwe,Ndi diso lace liona ciri conse ca mtengo wace.

11. Atseka mitsinje ingadonthe;Naturutsira poyera cobisikaci.

12. Koma nzeru, idzapezeka kuti?Ndi luntha, malo ace ali kuti?

Werengani mutu wathunthu Yobu 28