Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 28:25-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Pamene anaikira mphepo muyeso wace,Nayesera madzi miyeso;

26. Pakucitira mvula lamulo,Ndi njira yoyendamo mphezi ya bingu;

27. Pamenepo anaiona nzeru, naifotokozera;Anaikonza, naisanthula.

28. Koma kwa munthu anati,Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru;Ndi kupatukana naco coipa ndiko luntha.

Werengani mutu wathunthu Yobu 28