Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 28:20-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Koma nzeru ifuma kuti?Ndi luntha, pokhala pace pali kuti?

21. Popeza pabisikira maso a zamoyo zonse,Pabisikiranso mbalame za m'mlengalenga,

22. Cionongeko ndi Imfa zikuti,Tamva mbiri yace m'makutu mwathu.

23. Mulungu ndiye: azindikira njira yace,Ndiye adziwa pokhala pace.

Werengani mutu wathunthu Yobu 28