Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 28:18-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Korali kapena ngale sizikumbukikapo.Mtengo wace wa nzeru uposa wa korali wofiira.

19. Topazi wa Kusi sufanana nayo,Sailinganiza ndi golidi wolongosoka.

20. Koma nzeru ifuma kuti?Ndi luntha, pokhala pace pali kuti?

21. Popeza pabisikira maso a zamoyo zonse,Pabisikiranso mbalame za m'mlengalenga,

22. Cionongeko ndi Imfa zikuti,Tamva mbiri yace m'makutu mwathu.

23. Mulungu ndiye: azindikira njira yace,Ndiye adziwa pokhala pace.

24. Pakuti apenyerera malekezero a dziko lapansi,Naona pansi pa thambo ponse;

25. Pamene anaikira mphepo muyeso wace,Nayesera madzi miyeso;

26. Pakucitira mvula lamulo,Ndi njira yoyendamo mphezi ya bingu;

27. Pamenepo anaiona nzeru, naifotokozera;Anaikonza, naisanthula.

28. Koma kwa munthu anati,Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru;Ndi kupatukana naco coipa ndiko luntha.

Werengani mutu wathunthu Yobu 28