Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 28:17-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Golidi ndi krustalo sizilingana nayo;Ndi kusinthana kwace, siisinthanika ndi zisambiro za golidi woyengetsa.

18. Korali kapena ngale sizikumbukikapo.Mtengo wace wa nzeru uposa wa korali wofiira.

19. Topazi wa Kusi sufanana nayo,Sailinganiza ndi golidi wolongosoka.

20. Koma nzeru ifuma kuti?Ndi luntha, pokhala pace pali kuti?

21. Popeza pabisikira maso a zamoyo zonse,Pabisikiranso mbalame za m'mlengalenga,

22. Cionongeko ndi Imfa zikuti,Tamva mbiri yace m'makutu mwathu.

Werengani mutu wathunthu Yobu 28