Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 28:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma kuli mtapo wa siliva, Ndi malo a golidi amene amuyenga.

2. Citsulo acitenga m'nthaka,Ndi mkuwa ausungunula kumwala.

3. Munthu athawitsa mdima,Nafunafuna mpaka malekezero onse,Miyala ya mdima wa bii ndi ya mthunzi wa imfa.

4. Aboola mgodi posiyana patali pokhala anthu;Aiwalika ndi phazi lopitapo;Apacikika kutali ndi anthu, nalendewa-lendewa.

5. Kunena za nthaka, kucokera momwemo mumaturuka cakudya,Ndi m'munsi mwace musandulizika ngati ndi moto.

6. Miyala yace ndiyo malo a safiro,Ndipo iri nalo pfumbi lagolidi.

7. Njira imeneyi palibe ciombankhanga ciidziwa;Lingakhale diso la kabawi losapenyapo.

8. Nyama zodzikuza sizinapondapo,Ngakhale mkango waukali sunapitapo.

9. Munthu atambasulira dzanja lace kumwala;Agubuduza mapiri kuyambira kumizu.

10. Asema njira pakati pa matanthwe,Ndi diso lace liona ciri conse ca mtengo wace.

11. Atseka mitsinje ingadonthe;Naturutsira poyera cobisikaci.

12. Koma nzeru, idzapezeka kuti?Ndi luntha, malo ace ali kuti?

13. Munthu sadziwa mtengo wace;Ndipo silipezeka m'dziko la amoyo.

14. Pozama pakuti, Mwa ine mulibe;Ndi nyanja ikuti, Kwa ine kulibe.

15. Silipezeka ndi golidi,Sayesapo siliva mtengo wace.

Werengani mutu wathunthu Yobu 28