14. Akacuruka ana ace, ndiko kucurukira lupanga,Ndi ana ace sadzakhuta cakudya.
15. Akumtsalira iye adzaikidwa muimfa,Ndi akazi ace amasiye sadzalira maliro.
16. Cinkana akundika ndalama ngati pfumbi,Ndi kukonzeratu zobvala ngati dothi;
17. Azikonzeretu, koma wolungama adzazibvala,Ndi wosalakwa adzagawa ndalamazo.
18. Amanga nyumba yace ngati kadzoce,Ndi ngati wolindira amanga dindiro.
19. Agona pansi ali wacuma, koma saikidwa;Potsegula maso ace, wafa cikomo,
20. Zoopsa zimgwera ngati madzi;Nkuntho umtenga usiku.
21. Mphepo ya kum'mawa Imtenga, nacokaiye;Nimkankha acoke m'malo mwace.
22. Pakuti Mulungu adzamponyera zoopsa, osanlieka;Kuthawa akadathawa m'dzanja lace.