Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 27:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yobu anaonjezanso mwambi wace, nati,

2. Pali Mulungu, amene anandicotsera zoyenera ine,Ndi Wamphamvuyonse, amene anawawitsa moyo wanga,

3. Pakuti moyo wanga wonse ukali mwa ine,Ndi mpweya wa Mulungu m'mphuno mwanga;

4. Milomo yanga siilankhula cosalungama,Ndi lilime langa silichula zacinyengo.

5. Sindibvomereza konse kuti muli olungama;Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.

6. Ndiumirira cilungamo canga, osacileka;Cikhalire moyo ine, mtima wanga sunditonza.

7. Mdani wanga akhale ngati woipa,Ndi iye amene andiukira ngati wosalungama.

8. Pakuti ciyembekezo ca wonyoza Mulungu nciani pomlikhatu Mulungu,Pomcotsera moyo wace?

Werengani mutu wathunthu Yobu 27