Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 22:6-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Pakuti wamtenga cikole kwa mbale wako wopanda cifukwa,Ndi kubvula ausiwa zobvala zao.

7. Sunampatsa wolema madzi amwe,Ndi wanjala unammana cakudya.

8. Koma munthu mwini mphamvu, dziko ndi lace;Ndi munthu wobvomerezeka, anakhala momwemo.

9. Unabweza akazi amasiye osawaninkha kanthu,Ndi manja a ana amasiye anatyoledwa.

Werengani mutu wathunthu Yobu 22