26. Pakuti pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuyonse,Ndi kuweramutsa nkhope yako kwa Mulungu.
27. Udzampemphera ndipo adzakumvera;Nudzatsiriza zowinda zako.
28. Ukatsimikiza mtima kakuti, kadzakhazikikira iwe;Ndi kuunika kudzawala pa njira zako.
29. Anthu akakugwetsa pansi, udzati, Adzandikweza;Ndipo adzapulumutsa wodzicepetsayo.
30. Adzamasula ngakhale woparamula,Inde adzamasuka mwa kuyera kwa manja ako.