Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 22:15-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Udzasunga kodi njira yakale,Anaiponda anthu amphulupulu?

16. Amene anakwatulidwa isanafike nyengo yao,Cigumula cinakokolola kuzika kwao;

17. Amene anati kwa Mulungu, Ticokereni;Ndipo, Angaticitire ciani Wamphamvuyonse?

18. Angakhale Iye adadzaza nyumba zao ndi zabwino;Koma uphungu wa oipa unditalikira.

19. Olungama aciona nakondwera; Ndi osalakwa awaseka pwepwete,

20. Ndi kuti, Zoonadi, otiukirawo alikhidwa,Ndi zowatsalira, moto unazipsereza.

21. Uzolowerane ndi Iye, nukhale ndi mtendere;Ukatero zokoma zidzakudzera,

22. Landira tsono cilamulo pakamwa pace,Nuwasunge maneno ace mumtimamwako.

23. Ukabweranso kwa Wamphamvuyonse, udzamanga bwino;Ukacotsera cosalungama kutali kwa mahema ako.

24. Ndipo utaye cuma cako kupfumbi,Ndi golidi wa ku ofiri ku miyala ya kumitsinje.

25. Ndipo Wamphamvuyonse adzakhala cuma cako,Ndi ndarama zako zofunika.

26. Pakuti pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuyonse,Ndi kuweramutsa nkhope yako kwa Mulungu.

27. Udzampemphera ndipo adzakumvera;Nudzatsiriza zowinda zako.

Werengani mutu wathunthu Yobu 22