14. Mitambo ndiyo comphimba, kuti angaone;Ndipo amayenda pa thambo lakumwamba.
15. Udzasunga kodi njira yakale,Anaiponda anthu amphulupulu?
16. Amene anakwatulidwa isanafike nyengo yao,Cigumula cinakokolola kuzika kwao;
17. Amene anati kwa Mulungu, Ticokereni;Ndipo, Angaticitire ciani Wamphamvuyonse?
18. Angakhale Iye adadzaza nyumba zao ndi zabwino;Koma uphungu wa oipa unditalikira.
19. Olungama aciona nakondwera; Ndi osalakwa awaseka pwepwete,
20. Ndi kuti, Zoonadi, otiukirawo alikhidwa,Ndi zowatsalira, moto unazipsereza.
21. Uzolowerane ndi Iye, nukhale ndi mtendere;Ukatero zokoma zidzakudzera,
22. Landira tsono cilamulo pakamwa pace,Nuwasunge maneno ace mumtimamwako.