Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 22:10-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Cifukwa cace misampha ikuzinga.Ndi mantha akubvuta modzidzimutsa,

11. Kapena mdima kuti ungaone,Ndi madzi aunyinji akumiza.

12. Kodi Mulungu sakhala m'mwamba m'tali?Ndipo penyani kutalika kwace kwa nyenyezi, ziri m'talitali.

13. Ndipo ukuti, Adziwa ciani Mulungu?Aweruza kodi mwa mdima wa bii?

14. Mitambo ndiyo comphimba, kuti angaone;Ndipo amayenda pa thambo lakumwamba.

15. Udzasunga kodi njira yakale,Anaiponda anthu amphulupulu?

16. Amene anakwatulidwa isanafike nyengo yao,Cigumula cinakokolola kuzika kwao;

17. Amene anati kwa Mulungu, Ticokereni;Ndipo, Angaticitire ciani Wamphamvuyonse?

18. Angakhale Iye adadzaza nyumba zao ndi zabwino;Koma uphungu wa oipa unditalikira.

19. Olungama aciona nakondwera; Ndi osalakwa awaseka pwepwete,

20. Ndi kuti, Zoonadi, otiukirawo alikhidwa,Ndi zowatsalira, moto unazipsereza.

21. Uzolowerane ndi Iye, nukhale ndi mtendere;Ukatero zokoma zidzakudzera,

22. Landira tsono cilamulo pakamwa pace,Nuwasunge maneno ace mumtimamwako.

23. Ukabweranso kwa Wamphamvuyonse, udzamanga bwino;Ukacotsera cosalungama kutali kwa mahema ako.

24. Ndipo utaye cuma cako kupfumbi,Ndi golidi wa ku ofiri ku miyala ya kumitsinje.

25. Ndipo Wamphamvuyonse adzakhala cuma cako,Ndi ndarama zako zofunika.

Werengani mutu wathunthu Yobu 22