Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 21:3-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Mundilole, ndinene nanenso; Ndipo nditanena ine, sekani.

4. Kodi ine, kudandaula kwanga, ndidandaulira munthu?Ndipo ndilekerenji kupsa mtima?

5. Ndiyang'anireni, nimusumwe,Gwirani pakamwa panu.

6. Ndikangokumbukila ndibvutika mtima,Ndi thupi langa licita nyau nyau.

7. Oipa akhaliranji ndi moyo,Nakalamba, nalemera kwakukuru?

8. Mbeu zao zikhazikika pamodzi nao pankhope pao,Ndi ana ao pamaso pao,

9. Nyumba zao sizitekeseka ndi mantha,Ngakhale ndodo ya Mulungu siiwakhalira.

10. Ng'ombe yao yamphongo imakwera, yosakanika;Ng'ombe yao yaikazi imaswa, yosapoloza.

Werengani mutu wathunthu Yobu 21