Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 21:27-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Taonani, ndidziwa maganizo anu,Ndi ciwembu mundilingirira moipa,

28. Pakuti munena, Iri kuti nyumba ya kalonga?Ndi hema wokhalamo woipa ali kuti?

29. Simunawafunsa kodi opita m'njira?Ndipo simusamalira zotsimikiza zao?

30. Zakuti munthu woipa asungika tsiku la tsoka?Naturutsidwa tsiku la mkwiyo?

31. Adzamfotokozera ndani njira yace pamaso pace?Nadzamlipitsa ndani pa ici anacicita?

Werengani mutu wathunthu Yobu 21