Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 21:12-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ayimbira lingaka ndi zeze,Nakondwera pomveka citoliro.

13. Atsekereza masiku ao ndi zokoma,Natsikira m'kamphindi kumanda.

14. Koma adati kwa Mulungu, Ticokereni;Pakuti sitifuna kudziwa njira zanu.

15. Wamphamvuyonse ndiye yani kuti timtumikire?Ndipo tidzapindulanji pakumpemphera Iye?

16. Taonani, zokoma zao siziri m'dzanja lao;(Koma uphungu wa oipa unditalikira.)

17. Ngati nyali za oipa zizimidwa kawiri kawiri?Ngati tsoka lao liwagwera?Ngati Mulungu awagawira zowawa mu mkwiyo wace?

18. Ngati akunga ziputu zomka ndi mphepo,Ngati mungu wouluzika ndi nkuntho?

19. Mukuti, Mulungu asungira ana ace a munthu coipa cace,Ambwezere munthuyo kuti acidziwe.

20. Aone yekha cionongeko cace m'maso mwace,Namwe mkwiyo wa Wamphamvuyonse.

21. Pakuti comsamalitsa nyumba yace nciani, atapita iye,Ciwerengo ca miyezi yace citadulidwa pakati?

22. Ngati pali munthu wakumphunzitsa Mulungu nzeru?Popeza Iye aweruza mlandu iwo okwezeka.

23. Wina akufa, wabiriwiri,Ali cikhalire ndi cipumulire.

24. Mbale zace zidzala ndi mkaka;Ndi wongo wa m'mafupa ace uli momwe.

25. Koma mnzace akufa ali nao mtima wakuwawa,Osalawa cokoma konse.

26. Iwo agona cimodzimodzi kupfumbi,Ndi mphutsi ziwakuta.

27. Taonani, ndidziwa maganizo anu,Ndi ciwembu mundilingirira moipa,

28. Pakuti munena, Iri kuti nyumba ya kalonga?Ndi hema wokhalamo woipa ali kuti?

Werengani mutu wathunthu Yobu 21