Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 21:11-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Aturutsa makanda ao ngati gulu,Ndi ana ao amabvinabvina.

12. Ayimbira lingaka ndi zeze,Nakondwera pomveka citoliro.

13. Atsekereza masiku ao ndi zokoma,Natsikira m'kamphindi kumanda.

14. Koma adati kwa Mulungu, Ticokereni;Pakuti sitifuna kudziwa njira zanu.

15. Wamphamvuyonse ndiye yani kuti timtumikire?Ndipo tidzapindulanji pakumpemphera Iye?

16. Taonani, zokoma zao siziri m'dzanja lao;(Koma uphungu wa oipa unditalikira.)

17. Ngati nyali za oipa zizimidwa kawiri kawiri?Ngati tsoka lao liwagwera?Ngati Mulungu awagawira zowawa mu mkwiyo wace?

18. Ngati akunga ziputu zomka ndi mphepo,Ngati mungu wouluzika ndi nkuntho?

19. Mukuti, Mulungu asungira ana ace a munthu coipa cace,Ambwezere munthuyo kuti acidziwe.

20. Aone yekha cionongeko cace m'maso mwace,Namwe mkwiyo wa Wamphamvuyonse.

21. Pakuti comsamalitsa nyumba yace nciani, atapita iye,Ciwerengo ca miyezi yace citadulidwa pakati?

Werengani mutu wathunthu Yobu 21