Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 20:23-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Poti adzaze mimba yace,Mulungu adzamponyera mkwiyo wace waukali,Nadzambvumbitsira uwu pakudya iye.

24. Adzathawa cida cacitsulo,Ndi mubvi wa uta wamkuwa udzampyoza.

25. Auzula, nuturuka m'thupi mwace;Inde nsonga yonyezimira ituruka m'ndulu mwace;Zamgwera zoopsa.

26. Zamdima zonse zimsungikira zikhale cuma cace,Moto wosaukoleza munthu udzampsereza;Udzatha wotsalira m'hema mwace.

27. M'mwamba mudzabvumbulutsa mphulupulu yace,Ndi dziko lapansi lidzamuukira.

28. Phindu la m'nyumba mwace lidzacoka,Akatundu ace adzamthawa tsiku la mkwiyo wace.

29. Ili ndi gawo la munthu woipa, locokera kwa Mulungu,Ndi colowa amuikiratu Mulungu.

Werengani mutu wathunthu Yobu 20