Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 20:2-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. M'mwemo zolingirira zanga zindiyankha,Cifukwa cace ndifulumidwa m'kati mwanga.

3. Ndamva kudzudzula kwakundicititsa manyazi,Ndi mzimu wa nzeru yanga undiyankha.

4. Kodi sucidziwa ici ciyambire kale lomwe,Kuyambira anaika munthu pa dziko lapansi,

5. Kuti kupfuula kokondwera kwa woipa sikukhalira kutha,Ndi cimwemwe ca wonyoza Mulungu cikhala kamphindi?

6. Cinkana ukulu wace ukwera kumka kuthambo,Nugunda pamitambo mutu wace;

7. Koma adzatayika kosatha ngati zonyansa zace;Iwo amene adamuona adzati, Ali kuti iye?

8. Adzauluka ngati loto, osapezekanso;Nadzaingidwa ngati masomphenya a usiku.

9. Diso lidamuonalo silidzamuonanso;Ndi malo ace sadzampenyanso.

10. Ana ace adzapempha aumphawi awakomere mtima;Ndi manja ace adzabweza cuma cace.

11. Mafupa ace adzala nao unyamata wace,Koma udzagona naye pansi m'pfumbi.

12. Cinkana coipa cizuna m'kamwa mwace,Cinkana acibisa pansi pa lilime lace;

13. Cinkana acisunga, osacileka,Naoikhalitsa m'kamwa mwace;

14. Koma cakudya cace cidzasandulika m'matumbo mwace,Cidzakhala ndulu ya mphiri mkati mwace.

15. Anacimeza cuma koma adzacisanzanso;Mulungu adzaciturutsa m'mimba mwace.

16. Adzayamwa ndulu ya mphiri;Pakamwa pa njoka padzamupha.

Werengani mutu wathunthu Yobu 20