11. Mafupa ace adzala nao unyamata wace,Koma udzagona naye pansi m'pfumbi.
12. Cinkana coipa cizuna m'kamwa mwace,Cinkana acibisa pansi pa lilime lace;
13. Cinkana acisunga, osacileka,Naoikhalitsa m'kamwa mwace;
14. Koma cakudya cace cidzasandulika m'matumbo mwace,Cidzakhala ndulu ya mphiri mkati mwace.
15. Anacimeza cuma koma adzacisanzanso;Mulungu adzaciturutsa m'mimba mwace.
16. Adzayamwa ndulu ya mphiri;Pakamwa pa njoka padzamupha.
17. Sadzapenyerera timitsinje,Toyenda nao uci ndi mafuta.
18. Cimene adagwiriraco nchito, adzacibweza, osacimeza;Sadzakondwera monga mwa zolemera zace adaziona.