Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 2:7-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Naturuka Satana pamaso pa Yehova, nazunza Yobu ndi zironda zowawa, kuyambira ku phazi lace kufikira pakati pamutu pace.

8. Ndipo anadzitengera phale, kudzikanda nalo; nakhala pansi m'mapulusa.

9. Pamenepo mkazi wace ananena naye, Kodi uumiriranso kukhala wangwiro? citira Mulungu mwano, ufe.

10. Koma ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? pa ici conse Yobu sanacimwa ndi milomo yace.

11. Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za coipa ici conse cidamgwera, anadza, yense kucokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa.

12. Ndipo pokweza maso ao ali kutali, sanamdziwa, nakweza mau ao, nalira; nang'amba yense maraya ace, nawaza pfumbi kumwamba ligwe pamitu pao.

13. Nakhala pansi pamodzi naye panthaka masiku asanu ndi awiri usana ndi usiku, palibe mmodzi ananena naye kanthu, popeza anaona kuti kuwawaku nkwakukuru ndithu.

Werengani mutu wathunthu Yobu 2