Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 19:5-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ngati inu mudzikuza ndithu pa ine,Ndi kundichulira mtonzo wanga kuti munditsutse nao;

6. Dziwani tsopano kuti Mulungu wandikhotetsera mlandu wanga,Nandizinga ndi ukonde wace.

7. Taonani, ndipfuula kuti, Ciwawa! koma sandimvera;Ndikuwa, koma palibe ciweruzo.

8. Iye ananditsekera njira kuti ndisapitireko,Naika mdima poyendapo ine.

9. Anandibvula ulemerero wanga,Nandicotsera korona pamutu panga,

10. Nandigamula ponsepo, ndipo ndamukatu;Nacizula ciyembekezo canga ngati mtengo.

11. Wandiyatsiranso mkwiyo wace,Nandiyesera ngati wina wa adani ace.

12. Ankhondo ace andidzera pamodzi, nandiundira njira yao,Nandimangira misasa pozinga hema wanga.

13. Iye anandicotsera abale anga kutali,Ndi odziwana nane andiyesa mlendo konse.

14. Anansi anga andisowa,Ndi odziwana nane bwino andiiwala.

15. Iwo a m'nyumba mwanga ndi adzakazi anga andiyesa mlendo;Ndine wacilendo pamaso pao.

16. Ndikaitana kapolo wanga, sandibwezera mau,Cinkana ndimpembedza pakamwa panga.

17. Mpweya wanga unyansira mkazi wanga,Cinkana ndinampembedza ndi kuchula ana a thupi langa.

18. Angakhale ana ang'ono andipeputsa,Ndikanyamuka, andinena;

19. Mabwenzi anga eni eni onse anyansidwa nane;Ndi onse ndakondana nao asandulika adani anga.

Werengani mutu wathunthu Yobu 19