Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 19:18-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Angakhale ana ang'ono andipeputsa,Ndikanyamuka, andinena;

19. Mabwenzi anga eni eni onse anyansidwa nane;Ndi onse ndakondana nao asandulika adani anga.

20. Pfupa langa laumirira pa khungu langa ndi mnofu wanga,Ndipo ndapulumuka ndiri nazo nkhama za mano anga.

21. Ndicitireni cifundo, ndicitireni cifundo, mabwenzi anga inu;Pakuti dzanja la Mulungu landikhudza.

22. Mundilondola bwanji ngati Mulungu,Losakukwanirani thupi langa?

23. Ha! akadalembedwa mau anga!Ha! akadalembedwa m'buku!

24. Akadawazokota pathanthwe cikhalire,Ndi cozokotera cacitsulo ndi kuthira ntobvu!

25. Koma ndidziwa kuti Mombolo wanga ali ndi moyo,Nadzauka potsiriza papfumbi.

26. Ndipo khungu langa litaonongeka,Pamenepo wopanda thupi langa, ndidzapenya Mulungu;

27. Amene ndidzampenya ndekha,Ndi maso anga adzamuona, si wina ai.Imso zanga zatha m'kati mwanga.

28. Mukati, Tiyeni timlondole!Popeza cifukwa ca mlandu capezeka mwa ine;

29. Mucite nalo mantha lupanga; Pakuti mkwiyo utenga zolakwa za lupanga,Kuti mudziwe pali ciweruzo.

Werengani mutu wathunthu Yobu 19