1. Koma Yobu anayankha, nati,
2. Mudzasautsa moyo wanga kufikira liti,Ndi kundityolatyola nao mau?
3. Kakumi aka mwandicititsa manyazi;Mulibe manyazi kuti mundiumira mtima.
4. Ndipo ngati ndalakwa ndithu,Kulakwa kwanga kuli ndi ine ndekha.
5. Ngati inu mudzikuza ndithu pa ine,Ndi kundichulira mtonzo wanga kuti munditsutse nao;
6. Dziwani tsopano kuti Mulungu wandikhotetsera mlandu wanga,Nandizinga ndi ukonde wace.
7. Taonani, ndipfuula kuti, Ciwawa! koma sandimvera;Ndikuwa, koma palibe ciweruzo.
8. Iye ananditsekera njira kuti ndisapitireko,Naika mdima poyendapo ine.