Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 18:15-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Adzakhala m'hema mwace iwo amene sali ace;Miyala yasulfure idzawazika pokhala pace.

16. Mizu yace idzauma pansi,Ndi nthambi yace idzafota m'mwamba.

17. Cikumbukilo cace cidzatayika m'dziko,Ndipo adzasowa dzina kukhwalala.

18. Adzamkankha acoke ku kuunika alowe kumdima;Adzampitikitsa acoke m'dziko lokhalamo anthu.

19. Sadzakhala naye mwana kapena cidzukulu mwa anthu amtundu wace,Kapena wina wotsalira kumene anakhalako.

Werengani mutu wathunthu Yobu 18