Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 18:11-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Zoopetsa zidzamcititsa mantha monsemo,Nadzampitikitsa kumbuyo kwace.

12. Njala idzatha mphamvu yace,Ndi tsoka lidzamkonzekeratu pambali pace.

13. Zidzatha ziwalo za thupi lace,Mwana woyamba wa imfa adzatha ziwalo zace.

14. Adzazulidwa kuhema kwace kumene anakhulupirira;Nadzatengedwa kumka naye kwa mfumu ya zoopsa.

15. Adzakhala m'hema mwace iwo amene sali ace;Miyala yasulfure idzawazika pokhala pace.

16. Mizu yace idzauma pansi,Ndi nthambi yace idzafota m'mwamba.

17. Cikumbukilo cace cidzatayika m'dziko,Ndipo adzasowa dzina kukhwalala.

18. Adzamkankha acoke ku kuunika alowe kumdima;Adzampitikitsa acoke m'dziko lokhalamo anthu.

19. Sadzakhala naye mwana kapena cidzukulu mwa anthu amtundu wace,Kapena wina wotsalira kumene anakhalako.

20. Akudza m'mbuyo adzadabwa nalo tsiku lace,Monga aja omtsogolera anagwidwa mantha.

21. Zoonadi, zokhalamo osalungama zitero,Ndi malo a iye amene sadziwa Mulungu ndi awa.

Werengani mutu wathunthu Yobu 18