Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 18:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha, nati,

2. Musaka mau kufikira liti?Zindikirani, ndi pamenepo tidzanena.

3. Tiyesedwa bwanji ngati nyama za kuthengo,Ndi kukhala odetsedwa pamaso panu?

4. Iwe wodzing'amba mumkwiyo mwako,Kodi dziko lapansi lisiyidwe cifukwa ca iwe?Kapena thanthwe lisunthike m'malo mwace?

5. Inde, kuunika kwa woipa kudzazima,Ndi lawi la moto wace silidzawala.

6. Kuunikaku kudzada m'hema mwace,Ndi nyali yace ya pamwamba pace idzazima.

7. Mapondedwe ace amphamvu adzasautsidwa,Ndi uphungu wace wace udzamgwetsa.

8. Pakuti aponyedwa m'ukonde ndi mapazi ace,Namaponda pamatanda.

9. Msampha udzamgwira kucitende,Ndi khwekhwe lidzamkola.

10. Msampha woponda umbisikira pansi,Ndi msampha wa cipeto panjira.

Werengani mutu wathunthu Yobu 18