Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 16:16-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Nkhope yanga njodetsedwa ndi kulira misozi,Ndi pa zikope zanga pali mthunzi wa imfa;

17. Pangakhale palibe ciwawa m'manja mwanga,Ndi pemphero langa ndi loyera.

18. Dziko iwe, usakwirire mwazi wanga,Ndi kulira kwanga kusowe popumira.

19. Tsopanonso, taona, mboni yanga iri kumwamba,Ndi nkhoswe yanga ikhala m'mwamba.

20. Mabwenzi anga andinyoza; Koma diso langa lilirira misozi kwa Mulungu;

21. Ha! munthu akadapembedzera mnzace kwa Mulungu,Monga munthu apembedzera mnansi wace!

22. Pakuti zitafika zaka zowerengeka,Ndidzamuka ku njira imene sindibwererako.

Werengani mutu wathunthu Yobu 16