Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 15:6-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Pakamwa pako pakutsutsa, si ine ai.Inde milomo yako ikucitira umboni wakukutsutsa.

7. Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa?Kapena unayamba kulengedwa ndiwe, osati mapiri?

8. Kodi unamva uphungu wacinsinsi wa Mulungu?Ndipo unadzikokera nzeru kodi?

9. Udziwa ciani, osacidziwa ife?Uzindikira ciani, cosakhala mwa ife?

10. Pakati pa ife pali aimvi, ndi okalambitsa,Akuposa atate wako masiku ao,

11. Masangalatso a Mulungu akucepera kodi?Kapena uli naco cinsinsi kodi?

12. Mtima wako usonthokeranji nawe?Maso ako aphethira-phethira cifukwa ninji?

13. Kuti utembenuza mzimu wako utsutsane ndi Mulungu,Ndi kulola mau otere aturuke m'kamwa mwako.

14. Munthu nciani kuti akhale woyera,Wobadwa ndi mkazi kuti akhale wolungama?

15. Taona, Mulungu sakhulupirira opatulika ace;Ngakhale m'mwamba simuyera pamaso pace,

16. Koposa kotani nanga munthu wonyansa ndi wodetsa,Wakumwa cosalungama ngati madzi.

17. Ndidzakuonetsa, undimvere;Cimene ndinaciona, ndidzakufotokozera;

Werengani mutu wathunthu Yobu 15