18. Cimene adacinena anzeru,Adacilandira kwa makolo ao, osacibisa;
19. Ndiwo amene analandira okha dzikoli,Wosapita mlendo pakati pao;
20. Munthu woipa adzipweteka masiku ace onse,Ndi zaka zowerengeka zisingikira woopsa.
21. M'makutu mwace mumveka zoopsetsa;Pali mtendere amfikira wakumuononga.
22. Sakhulupirira kuti adzaturukamo mumdima,Koma kuti lupanga limlindira;
23. Ayendayenda ndi kufuna cakudya, nati, Ciri kuti?Adziwa kuti lamkonzekeratu pafupi tsiku lamdima,