1. Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,
2. Kodi mwini nzeru ayankhe ndi kudziwa kouluzika,Ndi kudzaza mimba yace ndi mphepo ya kum'mawa?
3. Kodi atsutsane ndi mnzace ndi mau akusathandiza?Kapena ndi maneno akusaphindulitsa?
4. Zedi uyesa cabe mantha,Nucepsa cilingiriro pamaso pa Mulungu.
5. Pakuti pakamwa pako paphunzitsa mphulupulu zako,Nusankha lilime la ocenjerera.