Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 13:24-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Mubisiranji nkhope yanu,Ndi kundiyesa mdani wanu?

25. Kodi mudzaopsa tsamba lakungouluka,Ndi kulondola ziputu zouma?

26. Pakuti mundilembera zinthu zowawa,Ndi kundipatsa ngati colowa mphulupulu za ubwana wanga.

27. Mulonganso mapazi anga m'zigologolo, ndi kupenyerera mayendedwe anga onse;Mudzilembera malire mopanika mapazi anga;

28. Momwemo munthu akutha ngati cinthu coola,Ngati cobvala codyedwa ndi numbi

Werengani mutu wathunthu Yobu 13