Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 13:11-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ukulu wace sukucititsani mantha,Ndi kuopsa kwace sikukugwerani kodi?

12. Zikumbutso zanu ndizo miyambi ya mapulusa;Zodzikanira zanu zikunga malinga adothi.

13. Khalani cete, ndilekeni, kuti ndinene,Condifikira cifike.

14. Ndilumirenji mnofu wanga pamano panga,Ndi kupereka moyo wanga m'dzanja langa?

15. Angakhale andipha koma ndidzamlindira;Komanso ndidzaumirira mayendedwe anga pamaso pace.

16. Iye adzakhalanso cipulumutso canga,Pakuti wonyoza Mulungu sadzafika pamaso pace.

17. Mvetsetsani mau anga,Ndi kunenetsa kwanga kumveke m'makutu mwanu.

18. Taonani tsono, ndalongosola mlandu wanga;Ndidziwa kuti adzandimasula ndiri wolungama,

19. Ndaniyo adzatsutsana nane?Ndikakhala cete, ndidzapereka mzimu wanga.

20. Zinthu ziwiri zokha musandicitire,Pamenepo sindidzabisalira nkhope yanu:

Werengani mutu wathunthu Yobu 13