Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 13:1-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Taonani; diso langa laciona conseci;M'khutu mwanga ndacimva ndi kucizindikira.

2. Cimene mucidziwa inu, inenso ndicidziwa;Sindikuceperani.

3. Koma ine ndidzanena ndi Wamphamvuyonse,Ndipo ndifuna kudzikanira kwa Mulungu.

4. Koma inu ndinu opanga zabodza,Asing'anga opanda pace inu nonse.

5. Mwenzi mutakhala cete konse,Ndiko kukadakhala nzeru zanu.

6. Tamvani tsono kudzikanira kwanga,Tamverani kudzinenera kwa milomo yanga.

7. Kodi munenera Mulungu mosalungama,Ndi kumnenera Iye monyenga?

8. Kodi mukhalira kumodzi ndi Iye?Mundilimbirana mwa Mulungu.

9. Ncokoma kodi kuti Iye akusanthuleni?Kodi mudzamnyenga Iye monga munyenga munthu?

10. Adzakudzudzulani ndithu,Mukacita tsankhu m'tseri.

11. Ukulu wace sukucititsani mantha,Ndi kuopsa kwace sikukugwerani kodi?

12. Zikumbutso zanu ndizo miyambi ya mapulusa;Zodzikanira zanu zikunga malinga adothi.

13. Khalani cete, ndilekeni, kuti ndinene,Condifikira cifike.

14. Ndilumirenji mnofu wanga pamano panga,Ndi kupereka moyo wanga m'dzanja langa?

15. Angakhale andipha koma ndidzamlindira;Komanso ndidzaumirira mayendedwe anga pamaso pace.

16. Iye adzakhalanso cipulumutso canga,Pakuti wonyoza Mulungu sadzafika pamaso pace.

Werengani mutu wathunthu Yobu 13