Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 12:15-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Taona atsekera madzi, naphwa;Awatsegulira, ndipo akokolola dziko lapansi.

16. Kwa Iye kuli mphamvu ndi nzeru.Wonyengedwa ndi wonyenga yemwe ali ace.

17. Apita nao maphungu atawafunkhira,Napulukiritsa oweruza milandu.

18. Amasula comangira ca mafumu,Nawamangira nsinga m'cuuno mwao.

19. Apita nao, ansembe atawafunkhica,Nagubuduza amphamvu.

20. Amcotsera wokhulupirika kunena kwace.Nalanda luntha la akulu.

21. Atsanulira mnyozo pa akalonga,Nawasezera olimba lamba lao.

22. Abvumbulutsa zozama mumdima,Naturutsa mthunzi wa imfa ukhale poyera;

23. Acurukitsa amitundu, nawaononganso;Abalalikitsa amitundu, nawabwezanso.

24. Awacotsera akulu a anthu a padziko mtima wao,Nawasokeretsa m'cipululu copanda njira.

25. Iwo ayambasa mumdima mopanda kuunika,Ndipo awayendetsa dzandi dzandi.

Werengani mutu wathunthu Yobu 12