Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 12:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Yobu anayankha, nati,

2. Zoonadi inu ndinu anthu,Ndi nzeru idzafa pamodzi ndi inu.

3. Koma inenso ndiri nayo nzeru monga inu.Sindingakucepereni;Ndani sadziwa zonga izi?

4. Ndine ngati munthu wosekedwa ndi mnansi wace,Ndinaitana kwa Mulungu, ndipo anandiyankha;Munthu wolungama wangwiro asekedwa.

5. Munthu wosatekeseka apeputsa tsoka mumtima mwace,Limlindira woterereka mapazi ace.

6. Mahema a acifwamba akhala mumtendere,Ndi iwo oputa Mulungu alimbika mtima:Amene Mulungu amadzazira dzanja lao.

7. Tafunsira tsono kwa nyamazo, zidzakulangiza,Ndi mbalame za m'mlengalenga, zidzakuuza;

8. Kapena ulankhule ndi dziko lapansi, lidzakulangiza;Ndi nsomba za kunyanja, zidzakufotokozera,

9. Ndaniyo sadziwa nazo izi zonse;Kuti dzanja la Yehova licita ici?

10. M'dzanja mwace muli mpweya wa zamoyo zonse,Ndi mzimu wa munthu ali yense.

11. M'khutumu simuyesa mau,Monga m'kamwa mulawa cakudya cace?

12. Kwa okalamba kuli nzeru,Ndi kwa a masiku ocuruka luntha.

13. Kwa Iye kuli nzeru ndi mphamvu;Uphungu ndi luntha ali nazo.

Werengani mutu wathunthu Yobu 12