Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 11:5-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Koma, hal mwenzi atanena Mulungu,Ndi kukutsegulira milomo yace motsutsa;

6. Nakufotokozere zinsinsi za nzeru,Popeza zipindika-pindika macitidwe ao!Cifukwa cace dziwa kuti Mulungu akuiwalira mphulupulu zina.

7. Kodi ukhoza kupeza Mulungu mwa kufunafuna?Ukhoza kupeza Wamphamvuyonse motsindika?

8. Kumpeza kutalika ngati kumwamba, ungacitenji?Kuzama ngati kumanda, ungadziwenji?

9. Muyeso wace utalikira utali wace wa dziko lapansi,Citando cace ciposa ca nyanja.

10. Akapita, nakatsekera,Nakaturutsa bwalo la mlandu, adzamletsa ndani?

11. Pakuti adziwa anthu opanda pace,Napenyanso mphulupulu, ngakhale saisamalira.

12. Koma munthu wopanda pace asowa nzeru,Ngakhale munthu abadwa ngati mwana wa mbidzi.

13. Ukakonzeratu mtima wako,Ndi kumtambasulira Iye manja ako;

14. Mukakhala mphulupulu m'dzanja lako, uicotseretu kutali,Ndi cisalungamo cisakhale m'mahema mwako;

15. Popeza pamenepo udzakweza nkhope yako opanda banga;Nudzalimbika osacita mantha;

16. Pakuti udzaiwala cisoni cako,Udzacikumbukila ngati madzi opita;

Werengani mutu wathunthu Yobu 11