Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 1:13-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Tsono panali tsiku loti ana ace amuna ndi akazi analinkudya ndi kumwa vinyo m'nyumba ya mkuru wao;

14. nafika mthenga kwa Yobu, nati, Ng'ombe zinalikulima, ndi aburu akazi analikudya pambali pao;

15. koma anazigwera Aseba, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.

16. Akali cilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Wagwa moto wa Mulungu wocokera kumwamba, wapsereza nkhosa ndi anyamata, nuzinyeketsa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.

17. Akali cilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Akasidi anadzigawa magulu atatu, nazigwera ngamila, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.

18. Akali cilankhulire, anadza winanso, nati, Ana anu amuna ndi akazi analinkudya ndi kumwa vinyo m'nyumba ya mkuru wao;

19. ndipo taonani, inadza mphepo yaikuru yocokera kucipululu, niomba pa ngondya zonse zinai za nyumbayo, nigwa pa anyamatawo, nafa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.

20. Pamenepo Yobu ananyamuka, nang'amba maraya ace, nameta mutu wace, nagwa pansi, nalambira,

21. nati, Ndinaturuka m'mimba ya mai wanga wamarisece, wamarisece ndidzanrukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.

22. Mwa ici conse Yobu sanacimwa, kapena kunenera Mulungu colakwa.

Werengani mutu wathunthu Yobu 1