Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 8:9-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Citani phokoso, anthu inu, koma mudzatyokatyoka; cherani khutu, inu nonse a maiko akutari; kwindani nokha, koma mudzatyokatyoka; kwindani nokha, koma mudzatyokatyoka.

10. Panganani upo, koma udzakhala cabe; nenani mau, koma sadzacitika; pakuti Mulungu ali pamodzi ndi ife.

11. Pakuti Yehova watero kwa ine ndi dzanja lolimba, nandilangiza ine kuti ndisayende m'njira ya anthu awa, nati,

12. Musacinene, Ciwembu; ciri conse cimene anthu awa adzacinena, Ciwembu; musaope monga kuopa kwao kapena musacite mantha.

13. Yehova wa makamu, Iye mudzamyeretsa; muope Iye, akucititseni mantha Iye.

14. Ndipo Iye adzakhala malo opatulika; koma mwala wopunthwitsa, ndi thanthwe lolakwitsa la nyumba zonse ziwiri za Israyeli, khwekhwe ndi msampha wa okhala m'Yerusalemu.

15. Ndipo ambiri adzapunthwapo, nagwa, natyoka, nakodwa, natengedwa.

16. Manga umboni, mata cizindikilo pacilamulo mwa aphunzi anga.

17. Ndipo ndidzalindira Yehova, amene wabisira a nyumba ya Yakobo nkhope yace, ndipo ndidzamyembekeza Iye,

18. Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa ine, tiri zizindikilo ndi zodabwitsa mwa Israyeli, kucokera kwa Yehova wa makamu, amene akhala m'phiri la Ziyoni.

19. Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Cifukwa ca amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?

20. Kucilamulo ndi kuumboni! ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbanda kuca.

21. Ndipo iwo adzapitirira obvutidwa ndi anjala, ndipo padzakhala kuti pokhala ndi njala iwo adzadziputa okha, ndi kutemberera mfumu yao, ndi Mulungu wao; ndi kugadamira nkhope zao kumwamba;

22. nadzayang'ana padziko, koma taonani, nkhawa ndi mdima, kuziya kwa nsautso; ndi mdima woti bi udzaingitsidwa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 8