Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 64:7-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo palibe amene aitana dzina lanu, amene adzikangamiza yekha kugwiritsa Inu; pakuti Inu mwatibisira nkhope yanu, ndipo mwatinyeketsa ndi zoipa zathu.

8. Koma tsopano, Yehova, Inu ndinu Atate wathu; ife tiri dongo, ndipo Inu ndinu Muumbi wathu; ndipo ife tonse tiri nchito ya dzanja lanu.

9. Musakwiye kopambana, Yehova, musakumbukire zoipa nthawi zonse; taonani, yang'anani ife, tikupembedzani Inu, ife tonse tiri anthu anu.

10. Midzi yanu yopatulika yasanduka cipululu, Ziyoni wasanduka cipululu, Yerusalemu wasanduka bwinja.

11. Nyumba yathu yopatulika ndi yokongola, m'mene makolo athu anakutamandani Inu, yatenthedwa ndi moto; ndi zinthu zathu zonse zokondweretsa zapasuka.

12. Kodi mudzadziletsa pa zinthuzi, Yehova? Kodi Inu mudzakhala cete ndi kutibvutitsa ife zolimba?

Werengani mutu wathunthu Yesaya 64