Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 6:4-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo maziko a ziundo anasunthika ndi mau amene anapfuula, ndipo nyumba inadzazidwa ndi utsi.

5. Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! cifukwa ndathedwa; cifukwa ndiri munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; cifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.

6. Pompo anaulukira kwa ine mmodzi wa aserafi, ali nalo khala lamoto m'dzanja mwace, limene analicotsa ndi mbaniro pa guwa la nsembe;

7. nakhudza nalo kukamwa kwanga nati, Taona ici cakhudza milomo yako; ndipo mphulupulu zako zacotsedwa, zocimwa zako zaomboledwa.

8. Ndipo ndinamva mau a Ambuye akuti, Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife? Ndipo ine ndinati, Ndine pano; munditumize ine.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 6