Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 59:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Taonani, mkono wa Yehova sufupika, kuti sungathe kupulumutsa; khutu lace siliri logontha, kuti silingamve;

2. koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo macimo anu abisa nkhope yace kwa inu, kuti Iye sakumva.

3. Pakuti manja anu adetsedwa ndi mwazi, ndi zala zanu ndi mphulupulu, milomo yanu yanena zonama, lilime lanu lilankhula moipa.

4. Palibe woturutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwacabe, nanena zonama; iwo atenga kusayeruzika ndi kubala mphulupulu,

5. Iwo afungatira mazira a mamba aswetse, naluka ukonde wa tandaude; iye amene adya mazira ace amafa, ndi coswanyikaco cisweka nicikhala songo.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 59