Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 58:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pfuula zolimba, usalekerere, kweza mau ako ngati lipenga, ndi kuwafotokozera anthu anga colakwa cao, ndi banja la Yakobo macimo ao.

2. Koma iwo andifuna Ine tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera kudziwa njira zanga; monga mtundu wa anthu ocita cilungamo, osasiya cilangizo ca Mulungu wao, iwo andipempha Ine zilangizo zolungama, nakondwerera kuyandikira kwa Mulungu.

3. Amati, Bwanji ife tasala kudya, ndipo Inu simuona? ndi bwanji ife tabvutitsa moyo wathu, ndipo Inu simusamalira? Taonani, tsiku la kusala kudya kwanu inu mupeza kukondwerera kwanu, ndi kutsendereza anchito anu onse.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 58