Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 5:9-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. M'makutu anga, ati Yehova wa makamu, Zoonadi nyumba zambiri zidzakhala bwinja, ngakhale zazikuru ndi zokoma zopanda wokhalamo.

10. Cifukwa kuti munda wamphesa wa madera khumi udzangobala mbiya imodzi, ndi mbeu za nsengwa khumi zidzangobala nsengwa imodzi.

11. Tsoka kwa iwo amene adzuka m'mamawa kuti atsate zakumwa zaukali; amene acezera usiku kufikira vinyo awaledzeretsal

12. Ndipo zeze ndi mgoli, ndi lingaka ndi citoliro, ndi vinyo, ziri m'mapwando ao; koma iwo sapenyetsa nchito ya Yehova; ngakhale kuyang'ana pa macitidwe a manja ace.

13. Cifukwa cace anthu anga amuka m'nsinga, cifukwa ca kusowa nzeru; ndi amuna ao olemekezeka ali ndi njala, ndi khamu lao lauma kukhosi.

14. Ndipo manda akuza cilakolako cace, natsegula kukamwa kwace kosayeseka; ndi ulemerero wao, ndi unyinji wao, ndi phokoso lao, ndi iye amene akondwerera mwa iwo atsikira mommo.

15. Munthu wonyozeka waweramitsidwa, ndi munthu wochuka watsitsidwa, ndi maso a wodzikweza atsitsidwa;

16. koma Yehova wa makamu wakwezedwa m'ciweruziro, ndipo Mulungu Woyera wayeretsedwa m'cilungamo.

17. Pamenepo ana a nkhosa adzadyapo ngati m'busa mwao, ndi malo a bwinja a zonenepa zacilendo zidzadyapo.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 5