Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 5:26-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo Iye adzakwezera a mitundu yakutari mbendera, nadzawayimbira mluzu, acokere ku malekezero a dziko; ndipo taonani, iwo adzadza ndi liwiro msanga msanga;

27. palibe amene adzalema, kapena adzapunthwa mwa iwo, palibe amene adzaodzera kapena kugona tulo; ngakhale lamba la m'cuuno mwao silidzamasuka, kapena comangira ca nsapato zao sicidzaduka;

28. amene mibvi yao ili yakuthwa, ndi mauta ao onse athifuka; ziboda za akavalo ao zidzayesedwa ngati mwala, ndi njinga zao ngati kabvumvulu;

29. kubangula kwao kudzafana ndi mkango, iwo adzabangula ngati ana a mikango, inde iwo adzabangula, nadzagwira nyama, naicotsa bwino opanda wakupulumutsa.

30. Ndipo iwo adzawabangulira tsiku limenelo ngati kukokoma kwa nyanja; ndipo wina ayang'ana padziko, taonani mdima ndi nsautso, kuyera kwadetsedwanso m'mitambo yace.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 5