9. Kumbukirani zinthu zoyamba zakale, kuti Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina wofana ndi Ine;
10. ndilalikira za cimariziro kuyambira paciyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanacitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzacita zofuna zanga zonse;
11. ndiitana mbalame yolusa kucokera kum'mawa, ndiye munthu wa uphungu wanga, kucokera ku dziko lakutari; inde, ndanena, ndidzacionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzacicitanso.
12. Mverani Ine, inu olimba mtima, amene muli kutari ndi cilungamo;