Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 33:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsoka kwa iwe amene usakaza, cinkana sunasakazidwa; nupangira ciwembu, cinkana sanakupangira iwe ciwembu! Utatha kusakaza, iwe udzasakazidwa; ndipo utatha kupangira ciwembu, iwo adzakupangira iwe ciwembu.

2. Inu Yehova, mutikomere ife mtima; ife talindira Inu; mukhale dzanja lathu m'mawa ndi m'mawa, cipulumutso cathunso m'nthawi ya mabvuto.

3. Pa mau a phokoso mitundu ya anthu yathawa; ponyamuka iwe amitundu abalalika,

4. Ndipo zofunkha zanu zidzasonkhanitsidwa, monga ziwala zisonkhana; monga madzombe atumpha, iwo adzatumpha pa izo.

5. Yehova wakwezedwa; pakuti akhala kumwamba; Iye wadzaza Ziyoni ndi ciweruzo ndi cilungamo.

6. Ndipo kudzakhala cilimbiko m'nthawi zako, cipulumutso cambiri, nzeru ndi kudziwa; kuopa kwa Yehova ndiko cumacace.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 33